Joshua 11

Kugonjetsedwa kwa Mafumu a Kumpoto

1Yabini, mfumu ya Hazori, inamva zimene zinachitikazi. Tsono inatumiza uthenga kwa Yobabu mfumu ya Madoni, ndiponso kwa mafumu a ku Simironi ndi Akisafu. 2Inatumizanso uthenga kwa mafumu a kumpoto, kumapiri, ndi mʼchigwa cha Yorodani kummwera kwa nyanja ya Kinereti, ndiponso kumadzulo mʼmbali mwa nyanja pafupi ndi Dori. 3Inatumizanso uthenga kwa Akanaani amene ankakhala kummawa ndi kumadzulo kwa Yorodani. Uthenga unapitanso kwa Aamori, Ahiti, Aperezi ndi Ayebusi amene amakhala mʼdziko la ku mapiri ndiponso kwa Ahivi amene ankakhala mʼmunsi mwa phiri la Herimoni ku chigwa cha Mizipa. 4Mafumuwo anabwera pamodzi ndi ankhondo awo onse. Gulu la ankhondo linali lalikulu ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Analinso ndi akavalo ndi magaleta ambiri. 5Mafumu onsewa anasonkhana pamodzi ndipo anamanga misasa yawo ku mtsinje wa Meromu, kuti amenyane ndi Israeli.

6Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.”

7Kotero Yoswa pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo anafika kwa adani awo aja ku mtsinje wa Meromu modzidzimutsa ndi kuwathira nkhondo. 8Yehova anawapereka mʼmanja mwa Israeli mwakuti anawagonjetseratu ndi kuwapirikitsa njira yonse mpaka ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti Maimu, ndiponso kummawa ku chigwa cha Mizipa. Onse anaphedwa popanda wopulumuka. 9Yoswa anawachita zimene Yehova analamula. Iye anadula matsinde a akavalo awo ndi kutentha magaleta awo.

10Pambuyo pake Yoswa anabwera nalanda mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. (Nthawi imeneyo mzinda wa Hazori unali wopambana mizinda ina yonse). 11Anapha aliyense wa mu mzindamo popanda wotsala wamoyo, ndipo mzinda wa Hazori anawutentha ndi moto.

12Yoswa analanda mizinda yonse ndi mafumu ake. Anthu onse anaphedwa ndi lupanga monga momwe analamulira Mose, mtumiki wa Yehova. 13Israeli sanatenthe mizinda yomangidwa pa zitunda, kupatula mzinda wa Hazori, umene Yoswa anawutentha. 14Aisraeli anatenga zinthu zonse za mʼmizindayi pamodzi ndi ziweto kuti zikhale zawo, koma anapha anthu onse ndi lupanga osasiyako ndi mmodzi yemwe wamoyo. 15Monga momwe Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamulira Yoswa ndipo Yoswa anachita chilichonse chimene Yehova analamulira Mose.

16Kotero Yoswa analanda dziko lonse: dziko la ku mapiri, dera lonse la Negevi, chigawo chonse cha Goseni, ndi chigwa chake chonse, chigwa cha Yorodani, dziko lonse la lamapiri la Israeli pamodzi ndi chigwa chake chomwe. 17Dziko lolandidwalo linayambira ku phiri la Halaki limene linali ku Seiri mpaka ku Baala-Gadi mʼchigwa cha Lebanoni, kumunsi kwa phiri la Herimoni. Yoswa anagwira ndi kupha mafumu a dziko lonselo 18atachita nawo nkhondo kwa nthawi yayitali. 19Palibe ngakhale ndi mfumu imodzi yomwe imene inachita mgwirizano wa mtendere ndi Aisraeli kupatula Ahivi okhala ku Gibiyoni. Koma mizinda ina yonse anachita kuyigonjetsa pa nkhondo. 20Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe.

21Pa nthawi imeneyi Yoswa anapita kukawononga Aanaki okhala mʼdziko lija la ku mapiri ku Hebroni, Debri, Anabu komanso madera onse a ku mapiri a Yuda ndi Israeli. Yoswa anawawononga onse pamodzi ndi mizinda yawo. 22Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsalako mʼdziko lonse la Israeli; komabe ku Gaza, ku Gati ndi Asidodi kokha ndi kumene anatsalako pangʼono. 23Choncho Yoswa anagonjetsa dziko lonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Tsono Yoswa analipereka kwa Aisraeli kuti likhale lawo, fuko lililonse gawo lake.

Anthu onse anapumula, osamenyanso nkhondo.

Copyright information for NyaCCL